Hosea 11

Chikondi cha Mulungu pa Israeli

1“Israeli ali mwana, ndinamukonda,
ndipo ndinayitana mwana wanga kuti atuluke mu Igupto.
2Koma ndimati ndikamapitiriza kuyitana
iwo amandithawa kupita kutali.
Ankapereka nsembe kwa Abaala
ndipo ankafukiza lubani kwa mafano.
3Ndi Ine amene ndinaphunzitsa Efereimu kuyenda,
ndipo ndinawagwira pa mkono;
koma iwo sanazindikire
kuti ndine amene ndinawachiritsa.
4Ndinawatsogolera ndi zingwe zachifundo cha anthu
ndi zomangira za chikondi;
ndinachotsa goli mʼkhosi mwawo
ndipo ndinawerama nʼkuwadyetsa.

5“Sadzabwerera ku Igupto,
koma Asiriya ndiye adzakhala mfumu yawo
pakuti akana kutembenuka.
6Malupanga adzangʼanima mʼmizinda yawo,
ndipo adzawononga mipiringidzo ya zipata zawo
nadzathetseratu malingaliro awo.
7Anthu anga atsimikiza zondifulatira Ine.
Ngakhale atayitana Wammwambamwamba,
sizidzatheka kuti Iye awakwezenso.

8“Kodi ndingakusiye bwanji iwe Efereimu?
Kodi ndingakupereke bwanji iwe Israeli?
Kodi ndingakuchitire bwanji zimene ndinachitira Adima?
Kodi ndingathe bwanji kukuchitira zimene ndinachitira Zeboimu?
Mtima wanga wakana kutero;
chifundo changa chonse chikusefukira.
9Sindidzalola kuti ndikulange ndi mkwiyo wanga woopsa,
kapena kutembenuka ndi kuwononga Efereimu.
Pakuti Ine ndine Mulungu osati munthu,
Woyerayo pakati panu.
Sindidzabwera mwaukali.
10Iwo adzatsatira Yehova;
Iye adzabangula ngati mkango.
Akadzabangula,
ana ake adzabwera akunjenjemera kuchokera kumadzulo.
11Adzabwera akunjenjemera
ngati mbalame kuchokera ku Igupto,
ngati nkhunda kuchokera ku Asiriya.
Ine ndidzawakhazikanso mʼnyumba zawo,”
akutero Yehova.

Tchimo la Israeli

12Efereimu wandizungulira ndi mabodza,
nyumba ya Israeli yandizungulira ndi chinyengo.
Ndipo Yuda wawukira Mulungu,
wawukira ngakhale Woyerayo amene ndi wokhulupirika.
Copyright information for NyaCCL